We’ve updated our Terms of Use to reflect our new entity name and address. You can review the changes here.
We’ve updated our Terms of Use. You can review the changes here.

Mafunso Ndi Mayankho Vol. 3: Khristu Ndi Ntchito Zake (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
1. Ungalape ndi kukhukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako? Maso anu sanaone makutu sanamve Palibe amadziwa zomwe Mulungu wakonza Kwa iwo womkonda Mulungu wazionetsa kwa ine (*2) Ungalape ndi kukhulupira Khristu Ungalape ndi kukhulupira ndi mphamvu zako ungakhulupilire Mulungu wazionetsa kwa ine Sitinalandire, mzimu wamdziko Koma mzimu wa kwa Mulungu Kuti tidziwe ndikumvetsa zomwe Mulungu watipatsa Mulungu wandipatsa ulele 1 Akolinto, chaputa 2 ndime 9 Palibe amadziwa zomwe Mulungu wakonza Kwa iwo omkonda Mulungu wazionetsa kwa ine Ayi sinadziwe za chipulumutso changa koma Khristu wazionetsa izi kwa ine
2.
2. Kodi chiyanjano ndi chani? Na na na na na na na na na na (*4) Chiyanjano Kodi chiyanjano ndi chani Chiyanjano Kodi chiyanjano ndi chani Na na na na na na na na na na Tapulumutsidwa kumkwiyo wa Mulungu Mwa mwana wake Na na na na na na na na na Chikondi chinaoneka tikadali ochimwa Tili ochimwa Khristu adatifera Na na na na na na na na na Khristu anasangalatsa Mulungu potifera ife mwalo mwathu Sangalalani mu ubale wa ife ndi Mulungu (*2) Aroma 5:8 mpaka 11 Sangalalani mu ubale wa ife ndi Mulungu (*2) Na na na na na na na na na
3.
3. Kodi anthu amapulumuka bwanji Khristu asanabwere? Abelo enoki, Nowa , Abrahamu, Isake, Yakobo, Sara, Yosefe Makolo a mose, Mose, Lahabe, Gidioni, Barati, Samisoni, Yefita Davide, Samueli ndi Aneneri Kuyang’anira ku mzinda Kufunitsitsa kumwamba Anthu onsewa anali mchikhulupiliro pakufa Sanalandire zolonjezedwa, anangoziona patali Anangoona ndi kuzilandira patali Kufunitsa ku mwamba Anthu ankapulumuka bwanji Khristu asanabwere amkapulumuka pokhulupira Kukhulupira mpulumutsi Heberi 11 Kukhulupira mpulumutsi
4.
4. Kodi anthu amawonetsa bwanji chikhulupiliro Khristu asanabwere? Mchikhulupiro Abelo anapeleka nsembe yabwino kuposa Kaini Iye anatengedwe wangwiro Mulungu anamuyamikira Chikhululukiro chinalipo bwanji Khristu asanabwere Chimkaoneka popeleka nsembe Yomwe mulungu analamula Msembeyi ikuimira ndani Khristu mwana wa nkhosa Khristu mwana wa nkhosa Wofera machimo a mdziko Onani mwana wankhosa ochotsa machimo a mdziko Yohane 1:29 A Heberi 11 vesi 4 Onani mwana wa Nkhosa ochotsa machismo mdziko Yohane 1:29 Khristu mwana wankhosa wachotsa machimo mdziko
5.
5. Kodi Khristu anakhala bwanji munthu, popeza iye ndi Mulungu mwana? Maria usaope Wapeza chisomo ndi Mulungu Udzakhala ndi pakati nudzabala mwana wa mmuna Udzamutcha dzina lake Yesu (*2) Adzakhala wamkulu Adzatchulidwa mwana wa wamkulu (*2) Adzakhala wamkulu Adzatchulidwa mwana wamkulu (*2) Ambuye adzampatsa ufumu wa Davite Adzalamulira nyumba ya Yakobo Ufumu wake sudzatha Ufumu wake sudzatha Maria usaope wapeza chisomo ndi Mulungu Kodi Khristu anakhala bwanji Munthu? Iye ponga Mulungu anakhala munthu pobadwa Ndi mphamvu ya mzimu woyera ndi thupi ndi moyo Mu mmimba mwanamwali Maria Luka 1:20 mpaka 33 Maria
6.
6. Kodi Yesu anachimwako? 2:22, I petro 2:22 Sanachimwe, sanachimwe M’mau ake munalibe chinyengo konse Kodi Yesu anachimwa? Ayi! Yesu anali wamgwiro
7.
7. Kodi Yesu anafa imfa yotani? Usadzikonde, Usadzitame Usaganize ndiwe ndiwe oposa onse Samala za ena osati iwe wekha Maganizo a Khristu khale mwa iwe Maganizo a Khristu akhale mwa iwe Okhala Mulungu mchilengedwe chake Ponga Mulungu sanachiyese, cholanda Khristu anadzichepetsa Anakhala kapolo Kubadwa monga munthu Anakhala kapolo Infa yotani Khristu anafa Imfa yowawa pamtanda Afilipi chaputala 2 Imfa ya manyazi Mulungu anamukweluza Kumpatsa dzina loposa onse Bondo ligwande, kamwa livomereza Khristu ndi Ambuye (*2) Ulemu kwa Mulungu, Ulemu kwa Atate
8.
8. Kodi ndi ntchito zanji Khristu anachita monga Mesiya olonjezedwa? Ntchito zanji Khristu anachita Monga Mesiya olonjezedwa Mneneri, Mbusa, mfumu Kwa ife, mwana wabadwa Mwana wa mamuna wapatsidwa Ndi ulamuliro uli pa phewa lache Adzatchedwa waumphungu odabwitsa Mulungu wamkulu , Tate wosatha Kalonga wa mtendere Tutu tulututu (*2) Ntichito zanji Khristu anachita Monga Mesiya olonjezedwa Mneneri, M’busa, Mfumu Yesaya vesi 6 chaputa 9 Kwaife mwana wapatsidwa Ndi ulamuliro uli pa phewa lache Adzatchedwa waumphungu odabwitsa Mulungu wamkulu Tate osatha Kalonga wa mtendere
9.
9. Kodi Khristu akhala bwanji Mneneri wako? Ndiphuzira chifuniro chake Khristu andiphuzitsa chifuniro chake Kuchoka mbuku la Yesaya 61 Khristu anawelenga Mzimu wa Ambuye uli pa ine Pakuti wandidzodza ndilalikire kwa osauka Kumasula a msinga Osaona kuti aone Kulimbikitsa ofooka Kukhazikitsa chaka chokomera Yehova Ndiphuzira chifuniro chake Khristu andiphuzitsa chifuniro chake Khristu ali bwanji mneneri Yohane 15 :15 Ndiphuzira chifuniro chake Khristu andiphuzitsa chifuniro chake Zonse ndaphuzira kwa a tate ndakudziwitsani Mzimu wa Ambuye ali pa ine Pakuti wandidzodza ndilalikire kwa osauka Kumasula msinga
10.
10. Kodi Khristu akhala bwanji wamsembe wako? Khristu ndi m’busa bwanji Anandifera Khristu ndi m’busa bwanji Andipemphelera Anatsuka machimo anga onse Anatsuka machimo anga onse andipemphelera Akwanilitsa kwa a muyaya Kupulumutsa obwera kwa Mulungu mwa iye (*2) Aheberi 7 vesi 25 andipemphelera (*2)
11.
11. Kodi Khristu akhala bwanji mfumu yako? Khristu ali mfumu bwanji? Khristu, olamula, ateteza Akhazikitsa ufumu wake mdziko Khristu ali mfumu bwanji? Mbuye woweluza Mbuye wolamula Ndiye wopulumutsa Mbuye ndi mfumu Mbuye ndowoweruza Mbuye ndi mfumu Yesaya 33 ndime 22
12.
12. Kodi ungalape ndi kukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako? Ungalape? Ungakhulupilire? Ungalape ndukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako? (*2) Maso sanawone, makutu sanamve Palibe amadziwa zomwe Mulungu wakonza kwa iwo womkonda Mulungu wazionetsa kwa ine Ndi mzimu wake wazionetsa kwa ine Ndingalape Ndingakhulupilire Ndingalape ndikukhulupilira Khristu ndi Mphamvu yako Sitinalandire mzimu wamdziko koma mzimu wa kwa Mulungu Kuti tikamvetse zomwe Mulungu watipatsa ulere Wandipatsa ulere 1 Akolinto 2 Wandipatsa ulere Ungalape? Ungakhulupilire

about

“Khristu ndi ntchito zake” ikufotokoza chifukwa chimene Mulungu anatuma Yesu. Ntchito imene Yesu adagwira kukwanilitsa chipulumutso chathu ndi zimene akuchitabe mpakana lero. Nyimbozi zikuphuzitsa zoona zokhazokha kuchokera mmau a Mulungu za chikhalidwe cha Yesu, ntchito zake (mu ufumu wa Mulungu) komanso m’mene anatilumikizitsira ndi Mulungu.
Zikomo

credits

released May 10, 2019

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account