We’ve updated our Terms of Use to reflect our new entity name and address. You can review the changes here.
We’ve updated our Terms of Use. You can review the changes here.

Mafunso ndi Mayankho Vol. 1: Mulungu ndi Chilengedwe (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
1. MLUNGU NDI NDANI? Mlungu ndi ndani? Mlungu ali yekhayo, wamoyo oona Ndiwaulemerero, wamphamvu amadziwa zonse, Namalenga wamkulu, ndi mbuye, wadziko—lonse Mulungu wabwino, oyera, osatha—wamuyaya, osasintha Mulungu ndi ndani? Osatha wamuyaya Mulungu wamuyaya wabwino, oyera, osatha osasintha. sitingamvetse ulemerero wa Mulungu Wamuyaya osasintha, wosaoneka, Mulungu yekhayo kukhale ulemu, kunthawi zonse. (1 Timothy 1 ndime 17) Kukhale ulemu, kunthawi zosatha Amen
2.
2. ANALENGA MULUNGU NDANI? Analenga Mlungu ndani? Analenga Mlungu ndani? Palibe anamulenga Palibe anamulenga Chorus Asanabadwe mapiri Musanalenge dzikoli Nthawi yosayamba mpaka yosatha Ndinu Mulungu (Masalimo 90 ndime 2)
3.
3. KODI MULUNGU ALI NDI CHIYAMBI? Kodi Mulungu ali ndi chiyambi? Ayi Mulungu ndi wamuyaya Woyera woyera Ambuye Amene analipo, alipo, adzakhalapo Woyera woyera ,ndi Ambuye Mulungu wamphamvu Analipo alipo adzakhalapo (Chivumbulutso 4 ndime 8)
4.
4. KODI MULUNGU ANGATHE KUFA? Kodi Mulungu angathe kufa? Ayi ndi wamuyaya Chorus 1 Kunthawi zanthawi zanthawi zamuyaya Ndi Mlungu wamoyo ndi mfumu yamuyaya (yeremiya 10; 10) Chorus 2 Zaka zanu zikhalira mibadwo mibadwo Zaka zanu sizifikira kuthaaaa (Masalimo 102 ndime 24 ndi ndime 27)
5.
5. KODI KULINSO MULUNGU WINA? Kodi kuli Mulungu wina? Ayi woona ndi m’modzi Kodi kuli Mulungu wina Mulungu ndi m’modzi yekha Pa Yesaya 45 Mulungu ati Ine ndine Yehova, popanda Ine palibe Mulungu Ine ndine Mulungu, palibenso wofananane Ine ndine Mulungu palibenso Palibe Mlungu opanda Ine Idzani kwa Ine mupulumuke Nonse padziko pakuti Ndine Mulungu Wolungama ndi mpulumutsi Idzani kwaine mupulumuke Nonse padziko poti Ndine Mulungu
6.
6. MULUNGU M’MODZI APEZEKA KANGATI? Mulungu m’modzi apezeka kangati? Mlungu m’modzi mwa atatu Mulungu m’modzi apezeka kangati? Mlungu m’modzi mwa atatu Chisomo cha Ambuye, Yesu Khristu, Chikondi cha Mulungu ndi Chiyanjano cha Mzimu Woyera chikhale ndi inu nonse 2 Akorinto 13 ndime 14 Chisomo cha mbuye Chikhale nanu
7.
7. MULUNGU MWA ATATU NDI NDANI? Mulungu mwa atatu ndi ndani? Mulungu mwatatuyo ndi Atate, Mwana Mzimu woyera Mukani phunzitsani anthu onse Ndi kuwabatiza m’dzina laTate, Mwana, ndi Mzimu Woyera (Mateyu 28 ndime 19)
8.
8. MULUNGU ALI KUTI? Ndingapite kuti kuzemba mzimu wanu Ndithawire kuti kuzemba kupezeka kwanu Ndingapite m’mwamba, muliko Ndingakoze kamalanga, pansi, muliko Mlungu ali ku? ponsepo Mlungu ali ku? Ponsepo Mulungu ali ponsepo Ndingakoze kamalanga pansi, muli konko (Masalimo 139 ndime 7 ndi 8) Mulungu ali ponseso.
9.
9. MUNGAONE MLUNGU? Mungaone Mlungu? Ayi, Mulungu ndi Mzimu, ndipo alibe Thupi ngati munthu Mungaone Mlungu? Ngakhale sindimuona Ndidziwa kuti, andiona nthawi zonse Ndine Mulungu wapafupi ,si Mlungu wa patali Ndani munthu angabisale, kuti ine Ndisamuone? Kodi sindidzala kumwamba ndi pansi Ati Yehova Yeremiya 23 ndime 23--24
10.
10. KODI MULUNGU ADZIWA ZONSE? Kodi Mlungu adziwa zonse? Inde adziwa zonse Palibe chobisika kwa Iye Maso ake ali panjira ya aliyense Napenya moponda mwake (Jobu 34:21) Maso a Mulungu ali ponsepo Ayang’ana abwino ndi oyipa (Miyambo 15 ndime 3)
11.
11. KODI MULUNGU ANGATHE ZONSE? Kodi Mulungu angathe zonse? Inde chifuniro chake choyera Ndi Mulungu zonse zotheka Mateyu 19 ndime 26 Kodi Mulungu angathe zonse Inde chifuniro chake choyera
12.
12. ANAKULENGA NDANI? Anakulenga ndani? Mulungu Ndidziwa anandilenga Pa Genesisi 1 ndime 27 Mau a Mulungu ati Analenga munthu mchifanizo chake Mchifanizo chake Mulungu Analenga mwamuna ndi mkazi Anakulenga ndani? Ndidziwa anandilenga
13.
13. ANAKULENGERANJI MULUNGU? Anakulengeranji Mlungu? Anakulengeranji Mlungu? Kodi udziwa? Anandilenga ndizimulemekeza Ndikukondwera naye nthawi zonse Chorus Mungakhale mudya kapena kumwa Kaya muchita kanthu kena Chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu Chorus Ndingakhale ndidya kapena kumwa Kaya ndichita kanthu kena Ndichite zonse ku ulemerero wa Mulungu ( 1 Akorinto 10 ndime 31) Anandilenga ndizimulemekeza
14.
14. NDI CHANINSO CHOMWE MULUNGU ANALENGA? Ndichaninso chomwe Mulungu analenga? Mulungu analenga zinthu zonsezi Chorus Pachiyambi Mulungu analenga Kumwamba ndi pansipa Analenga kuwala usana ndi usiku, thambo ndi Nyanja Ndi zomera zonse Kenako chopambana Analenga munthu M’chifanizo chake analenga Mwamuna ndi mkazi (Genesisi mutu woyamba)
15.
15. MULUNGU ANALENGERANJI ZONSEZI? Mlungu analenganji zonse? Ulemerero wake Chifukwa cha ulemerero wake Analenga zonsezi Zonse zichokera kwa Iye Zichitika kufikira kwa Iye Ulemerero kunthawi zonse Aroma 11 ndime 36 KwaIye Ulemerero Kunthawi zonse Amen.
16.
16. UNGATAMANDE BWANJI MLUNGU? Ungatamande Bwanji Mlungu? Ndingatamande po mukonda Ndikuchita zomwe walamula Wakuonetsa Munthuwe chifundo Zabwino ndinso Ambuye afuna kwa iwe kuchitachilungamo Ndi kukonda chifundo Kudzichepetsa ndi Mulungu wako (Mika 6 ndime 8)
17.
17. CHIFUKWA CHANI NDILEMEKEZE MLUNGU? Lemekezani Yehova Amitundu nonse padziko Chikondi chake n’chachikulu Kwa ife (Masalimo 117) Chifukwa chiani ndilemekeze Mlungu? Ndizimulemekeza Chifukwa chiani ndilemekeze Mlungu anandilenga Chifukwa chiani ndilemekeze Mlungu Andisamalira Ndilemekeze Mlungu wanga
18.
18. MAKOLO ATHU OYAMBA NDANI? Makolo oyamba ndani? Adamu ndi Hava Adamu ndi Hava ndi makolo oyamba Chorus Kenako Mulungu anati Sibwino munthu akhale yekha Ndimpangira womuthangatira Ndipo analenga mkazi napita naye kwa mamuna Anamutcha Hava m’mayi wa anthu onse (Genesisi 2 ndi 3)
19.
19. MULUNGU ANAWUMBA BWANJI ADAMU NDI HAVA? Mulungu adawumba bwanji Adamu ndi Hava? Mulungu anawumba Adamu ndi dothi lapansi, adawumba bwanji Adamu ndi Hava? Mulungu anawumba Adamu ndi dothi lapansi, Napanga Hava ku mthiti ya Adamu Genesisi 2 ndime 7 anawumba munghu ndi dothi la pansi Genesisi 2 ndime 22 napanga mkazi ku mthiti ya mamuna
20.
20. ANAPEREKA CHIANI MULUNGU KWA ADAMU NDI HAVA PAMWAMBA PA THUPI?  Anapereka chiani kwa Adamu ndi Hava pamwamba pa thupi? Mulungu anawapatsa mzimu womwe sudzafa Anapereka chiani kwa Adamu ndi Hava pamwamba pa thupi? Mulungu anawapatsa mzimu womwe sudzafa Ambuye anapanga muthu kuchoker ku dothi lapansi Nauzira munthuo mpweya wa moyo Ndipo munthu anakhala wamoyo Mulungu anamuuzira mpweya wa moyo Genesisi 2 ndime 7 Mulungu anamuuzira mpweya wa moyo
21.
21. KODI ULI NDI MZIMU NDIPONSO THUPI? Kodi uli ndi mzimu ndiponso thupi? Inde mzimu womwe sudzafa Kodi uli ndi mzimu ndiponso thupi? Inde mzimu womwe sudzafa Mlaliki 12 ndime 7 Fumbi ku fumbi Mzimu kubwerera kwa Mulungu anaupereka
22.
22. KODI ADAMU NDI HAVA MULUNGU ANAWALENGA OTANI? Kodi Adamu ndi Hava Mulungu anawalenga otani? Anawalenga amgwiro ndi okondwa Genesis 2 ndime 25 Onse anali okondwa Genesis 2 ndime 25 Anali okondwa opanda manyazi

about

Find out how you can help support our ongoing work in Malawi by visiting songsforsaplings.com/missions/chichewa

This is the Chichewa version of "Questions with Answers Vol. 1: God and Creation"

credits

released October 10, 2010

Singers:
Linda Chiyani
Levi Dannayo
Gerald Chimkoka

Numeri Mwale
Calrorine Mwale

Michelle Chipingu
Jerush Chipingu

African Drums:
Levi Dannayo

Recording Engineer:
Matthew H. Curl

Place of recording:
African Bible College in Malawi

songsforsaplings.com/missions/chichewa

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account