We’ve updated our Terms of Use to reflect our new entity name and address. You can review the changes here.
We’ve updated our Terms of Use. You can review the changes here.

Mafunso Ndi Mayankho Vol. 4: Mau A Mulungu (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
1. Usakhale nayo Milungu ina koma ine ndekha Tsono Mose anatsika kuphiri Kupita kwa anthu Anachoka kuphiri anati Mulungu wanena izi kwa inu (*2) Ndinakuchotsani m’dziko la iguputo dziko la ukapolo Musakhale ndi milungu ina koma ine Musakhale ndi milungu ina, ine ndekha Tsono Mose anatsika kuphiri Kupita kwa anthu Anachoka kuphiri anati Mulungu wanena izi kwa inu Mulungu wanena izi kwa inu Mose anatsika, kutsika kuphiri Ekisodo 20 Anatsika kuphiri anati Mulungu wanena izi kwa inu
2.
2. Usadzipangire iwe wekha fano losema Chifundo, chikondi Ku zikwi zamibadwo Za ondikonda Chifundo, chikolndi Ku zikwi zamibadwo za osunga malamulo Usapange fanizo la chilichonse Osagwada ndikulambira Poti ndine Ambuye Mulungu wako Mulungu wa nsanje Olanga ana Kamba ka tchimo la kholo lawo Kwa mibadwo ndi mibadwo ya ondida ine
3.
3. Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe Oo mpatseni Ambuye, inu ana amphamvu Ulemu ndi mphamvu kwa Yehova Mpatseni Ambuye, dzina lake la ukulu Dzina lake la ukulu mu mchiyero chake Mlambireni Oo liwu la yehova liri pa madzi Ulemelero ugunda ku mapiri Ulemelero ulu pamadzi onse Oo Liu la Yehova lalikulu Usatenge dzina la Ambuye pachabe Muchiyero chake mlambireni Mpatseni Ambuye Dzina lake la ukulu Masalimo 29:2 Mlambireni
4.
4. Tsiku la Sabata Tsono pali lasabata la anthu, la anthu a Mulungu Poti Mulungu analenga kumwamba ndi dziko anapuma lasabata kuntchitozo Iye opuma mwa Mulungu apuma mu zintchitozo Yesetsani kupuma mwa iye kuti musagwe Poti tili ndi wa msembe Ali kwa iye, yesu mwana wa Mulungu Tiyeni tigwiritse chikhulupiliro tili nacho Anayesedwa ngati ife, opanda tchimo Tifikere mpando wachisomo ndiungwiro Kuti tilandire chifundo tikachifuna Puma mwa Yesu, puma mwa Yesu A heberi chaputala 4 Wansembe wathu mwana mwa Mulungu, mwana mwa Mulungu, wamsembe wathu mwana wa Mulungu
5.
5. Lemekeza atate ako ndi amako Ananu mverani makolo mwa Ambuye izi mzabwino Lemekezani bambo ndi mayi Ili ndi lamulo la lonjezo (*2) Kuti zikuyendereni mukhale ndi moyo wautali Kuti zikuyendereni Aefeso 6 vesi 1 Ananu mverani makolo mwa Ambuye izi Mzabwino Lemekeza bambo ndi mayi Ili ndi lamulo la lonjezo Lemekeza bambo ndi mayi Ili ndilamulo la lonjezo
6.
Usaphe 01:51
6. Usaphe Tidziwa tachoka ku imfa Chifukwa timakondana Aliyense osakonda ali mu imfa Aliyense oda mnzake waphwanya lamulo Usaphe Waphwanya lamulo Usaphe Ndi momwe tadziwira chikondi Yesu anatifelafe Ndipo tiyenera kufera anzathu 1 Yohane 3:14 Kondanani
7.
7. Usachite dama Imwa madzi a mchitsime chako ndi mkasupe wako Kodi magwero ako amwazike M’mitsinje m’makwalala Ikhale a iwe wekha Osati ndi alendo okhala nawe Kondwa ndi mkazi wako wa ubwana monga mbalawa Yokondwa ndi chinkhoma cha chisomo Miyambo 5:15 mpaka 19 Imwa madzi a chitsime ndi a kapuse wako Usapange nawo zadama Khala oyera m’tima, m’maganizo Konda mwamuna wako Khala oyera Usapange nawo za dama Khala oyera m’tima, m’maganizo Konda mkazi wako khala oyera
8.
Usabe 01:42
8. Usabe Iwe usabe, iwe usabe Iwe wakuba usabeso Usabeso kwa m’bale wako Usabeso Usabeso kwanzako onse Usabeso Iwe usabe, iwe usabe Aefeso 4 vesi 28 usabeso Koma ugwire ntchito mwachilungamo Usabeso Ndipo agawire kwa osowa Usabeso
9.
Usaname 01:45
9. Usaname Usaname Ambuye adana ndi onama (*3) Koma akondwera mwa munthu Oo Mbuye akondwera mwa munthu Miyambo 12:22 Wachilungamo
10.
Usasilire 01:29
10. Usasilire Khutitsidwa ndi zako Khutitsidwa ndi zako Khutitsidwa ndi zako Khutitsidwa Usasilire Usasilire nyumba ya mzako Usasilire mkazi wa m’nzako Usasilire n’gombe ya m’nzako Usasilire chilichonse chomwe ndi chamzako Uuuuuu uuuuu uuuuuu Mulungu anati Simdza, simdza, simdzakusiya Simdza, simdza, simdzakutaya Simdza, simdza simdzakusiya Simdza (*2) Heberi 13 vesi 5 (*4) Khutitsidwa
11.
11. Kodi tiphuzira kuti kukonda ndi kumvera Mulungu? Tiphunzira kuti kukonda? Tiphunzira kuti kumvera Mulungu? Tiphunzira kuti kukonda n’kumvera Mulungu? Mu Baibulo tiphunzira kukonda Mu Baibulo tiphunzira kumvera Mulungu Mu Baibulo tiphunzira kukonda n’kumvera Mulungu Sunga buku lachilamulo pakamwa pako Liwerenge tsiku ndi tsiku Kuti usamale mkuchita zonse zolembedwamo Yoswa chaputala 1 vesi 8
12.
12. Analemba Baibulo ndi ndani? Mzakukumbutsani nthawi zones za izi Ndingakhale m’dziwe muli mchilungamo Muli maso koma mdzakupatsani kupeza kwa bwino Kukupatsa mpaka kuchoka msasa omwe ndili nawowo Uuuuuuuuu uuuuuuuuu uuuuuuuwaaaaa Ndipo mumvetsere bwino za izi mpaka kuwala mu mdima Kuwala mu mdima Ndipo inu mumvetsere bwino za izi mpaka kuwala kwa mawa Mpaka nyali iwale mu mitima yanu Uuuuuuuuuuu uuuuuuuu uuuuuuwaaa Analemba Baibulo anthu a Mulungu Osankhidwa ndi Mulungu Analemba Baibulo anthu a Mulungu Owuzidwa ndi Mzimu oyera 2 Petro 1 Anthu analankula Monga mwa mzimu oyera
13.
13. Kodi lamulo la likulu ndi liti? Phuzitseni lamulo lalikulu mchani? Konda Mulungu ndi mtima, moyo n’zeru zako Phuzitseni lamulo lalikulu n’chani Konda m’nzako ndi lamulo la chiwiri (*2) Konda Ambuye Mulungu Ndi mtima wako Konda Ambuye Mulungu Ndi moyo wako Konda Ambuye mulungu Ndi nzeru zako Kondaso mzako ndi mtima onse Chiphatikizo chonse Mateyu 22 ndime 36 Chiphatikizo chonse
14.
14. Kodi Mulungu amakondwela ndi omukonda komanso omumvera? Ndikonda ondikonda Ndipo ondifuna adzandipeza Ndikonda ondikonda Miyambo 8 vesi 17 (*2) Iye osunga malamulo anga Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda Adzakondedwa ndi atate anga Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda Ndidzakondanso, ndizakonda Amakondanso amakonda Ndidzazionetsera kwa iye Ndiye okonda Ndikonda ondikonda Ndipo ondifuna adzandipeza Ndikonda ondikonda Miyambo 8 vesi 17 Iye osunga malamulo anga Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda Adzakondedwa ndi Atate anga Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda Mulungu akondwa omukonda ndi omvera? Amakondanso omukonda Yohane 14 vesi 21 Ndiye ondikonda
15.
15. Kodi Mulungu sakondwela ndi omuda komanso osamumvera? Masalimo chaputala 7:9 mpaka 11(*2) Atate wa mwamba odziwa iso ndi mtima Thetsani nkhondo zaoipa nditetezeni Chida changa ndinu Mupulumutsa oongoka, oweruza wangwiro Mumva mkwiyo nthawi zones Oooooh owuhooooo hoooo Mulungu sakondwera ndi omuda iye Amakwiya ndi woipa nthawi zonse Mulungu sakondwera ndi osamvera? Amakwiya ndi woipa nthawi zonse Musang’ambe zovala zanu muchisoni Koma mitima, bwererani kwa Ambuye Ngwachifundo, chikondi, wosakwiya nsanga Ngokhululuka, ali chile kuleza Yoweli 2:13
16.
16. Kodi malamulo khumi ndi antchito yanji? Chani? Bwanji?, ndiyese? Zabwino bwanji? Zabwino bwanji kwa ine?(*2) Kuti zindiphuzitse ntchito, kwa anthu ndi kwa Mulungu okhala oyera Monga Mulungu Deturonome 29 Zodziwika kwa ife ndi ana athu mpaka kale Chani? Bwanji?, ndiyese? Zabwino bwanji? Zabwino bwanji kwa ine? (*2) kuti zionetse kufuna kwathu ife Tifunitsa mpulumutsi, mpulumutsi Kuti titsate chilamulo Deturonomo 29:29

about

Mau a Mulungu ali ndi nyimbo zomwe zimathandizira kuphuzitsa Malamulo khumi a Mulungu komanso lamulo loposa ndi kufunikira kwakwe kwa izi. Nyimbo zina zoonjezera zikufotokoza m’mene mulungu anatipatsira ndi chifukwa chomwe anatipatsira Baibulo. Likufotokozanso chifukwa chomwe tiyenera kulikhulupilira komanso kuti ndilofunika bwanji kwa ife.
Zikomo

credits

released May 10, 2019

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account