We’ve updated our Terms of Use to reflect our new entity name and address. You can review the changes here.
We’ve updated our Terms of Use. You can review the changes here.

Mafunso ndi Mayankho Vol. 2: KUGWA NDI CHIPULUMUTSO (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
1. CHIPANGANO NDI CHANI? Ndi Ambuye ndi Ambuye Ndi Ambuye Mulungu wathu Maweruzo ake ali padziko Akumbukira chipangano kwa muyaya Mau anawalamulira, mibadwo zikwi (Masalimo 105: 7 ndi 8)   Ndi Ambuye ndi Ambuye Mulungu wathu   Chipangano ndi chiani? Mgwirizano Mulungu apanganafe Omwe atsimikiza kusunga Kusunga Lonjezo Lake Kusunga Lonjezo Lake
2.
2. GAWO LA ADAM MU CHIPANGANO KUTI AKHALEBE MMUNDA WA EDENI NLITI? Gawo la Adamu muchipangano Kuti akhalabe mmunda wa Edini nliti Adamu ayenera kumvera Mlungu wangwiro Ndipo Yehova anati kwa munthu Mitengo yonse ya mmundayo udye Koma usadye mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa Usadye mtengo wakudziwitsa zabwino ndizoipa Chifukwa ukadya udzafa ndithu (Genesis 2: 15 mpaka 17)
3.
3. KODI ADAMU ADAMVERA MULUNG? Kodi Adamu adamvera Mulungu? Ayi Adamu adasankha kusamvera Mlungu Adamu adasankha kusamvera   Mmene mkazi anaona chipatso Chinali chabwino kudya, chokongola m’maso Chipatso cholakalakika kupatsa nzeru Anatenga chipatso nadya napatsa Mwamuna anali naye nadya (Genesisi 3 ndime 6) Adamu anasankha kusamvera
4.
4. MULUNGU ANALANGA KUSAMVERA KWA ADAMU MOTANI? Minga, zilonda ndi minga, zilonda ndi minga Zilonda yotembereredwa nthaka Minga, zilonda ndi minga, zilonda ndi minga, Zilonda masiku a moyo wonse   Zowawa, zokhoma, zowawa, zokhoma Zowawa zokhoma udzadya m’menemo Zowawa zokhoma zowawa zokhoma Zowawa masiku a moyo onse Kuchotsedwa m’munda wa Edeni Kugwira ntchito mnthaka yomwe anachokera Kupirikitsidwa m’munda wa Edeni Olondedwa ndi lupanga la moto Mulungu analanga kusamvera kwa Adamu motani? Chilango cha Adamu chinali Imfa ndi kulekana ndi Mulungu (Genesisi 3 ndime 17 mpaka 24)
5.
5. TCHIMO NDI CHANI? Chifundo chanu, Kumbukirani nsoni zanu Mbuye, Kukoma mtima kwanu Chifundo chanu, pakuti izi Nzakale lonse, chifundo ndi chikondi chanu Musakumbukire zolakwa za ubwananga zopikisana nanu Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu Chifukwa chaubwino wanu Tchimo ndi chani? Tchimo ndi kusamvera chilamulo cha Mulungu, Polephera kupanga zotilamulira Kapena kupapanga zoletsedwa ndi Mulungu (Masalimo 25 ndime 6 ndi 7) Chifundo chanu
6.
6. SATANA NDI NDANI? Dziletseni dziletseni dziletseni dikirani Dziletseni dziletseni dziletseni dikirani M’dani wanu Satana ayenda ngati mkango Kufuna womulikwira   Satana ndi ndani? Satana ndi mzimu woyipa Wodana ndi Mulungu ndi Akhristu (1 Petro 5 ndime 8) Dziletseni dikilani
7.
7. WAMKULU NDANI MULUNGU NDI SATANA? Wamkulu ndi ali mwa inu Kuposa ali m’dziko   Wamphamvu ndani Mulungu kapena Satana? Mulungu ndiye wamphamvu Ndinu ochokera kwa Mulungu Mwapambana iwo a mdziko (1 Yohane 4:4)
8.
8. KODI TCHIMO LA MAKOLO ATHU OYAMBA NDI LITI? Gene Gene Gene Genesis 3 vesi 6 Gene Gene Gene Genesis 3 vesi 6 munthu anachimwa pa Genesisi 3 vesi 6 Tchimo lamakolo oyamba nliti? Kudya chipatso choletsedwa Kudya chipatso choletsed
9.
9. ANAMUYESA ADAMU NDI HAVA KUTI ACHIMWE NDI NDANI? Anamuyesa Hava? Anamuyesa Adamu ? Anamuyesa Adamu ndi Hava ndani? Satana anayesa Hava Nampatsa chipatso adamu Adamu chipatso na chidya   Pa Genesis 3 Njoka inati kwa mkazi Simudzafa yi Mulungu adziwa maso anu adzatsekuka Mudzakhala ngati Mulungu, Wodziwa zabwino ndi zoipa Mudzakhala ngati Mulungu
10.
10. CHINACHITIKA NCHIYANI KWA ADAMU NDI HAVA ATACHIMWA? Chinachitika n’chiani kwa Adamu ndi Hava atachimwa? M’malo mokhala oyera ndi okondwa Anakhala ochimwa ndi ovutika Odziwa zabwino ndizoyipa Genesisi 3:22 Zabwino ndi zoipa
11.
11. KODI TCHIMO LA ADAMU LINAKUTANI? Tchimo la adamu linakuta ni Linandipanga womanyazi ndi wochimwa Monga mmene tchimo linalowela mdziko Mwa munthu, imfa mwa tchimo Momwemonso imfa inabwera kwa munthu Chifukwa cha tchimo na na na na na na na n Imfa ndi Adam moyo ndi Khristu Aroma 5:12
12.
12. KODI TCHIMO LILILONSE LITITENGERA CHIYANI? Tchimo litlitengera chiyani? Mkwiyo wa Mulungu Temberero la Mlungu   Ana akataya chilamulo Osayenda m’maweruzo anga Nakaipsa malemba anga osasunga malamulo, Ndidzalanga tchimo lawo Masalimo 89 ndime 30 mpaka 32
13.
13. KODI NDIWE OCHIMWA MOTANI MWACHIKHALIDWE? Palibe mmodzi Palibe inde ngakhale m’modzi Palibe oyera Palibe mmodzi Palibe amene amvetsetsa Afuna Mulungu Palibe mmodzi Apatuka alowerera Palibe m’modzi wochita zabwino, olo m’modzi Ochimwa mwachibadwe Palibe oyera Ndiwe woipitsitsa mmagawo onse Afuna Mulungu Palibe Aroma 3 ndime 11 mpaka 12 Palibe m’modzi wochita zabwino, olo m’modzi
14.
14. KODI UNGAPITE KCHUMWAMBA NDI CHIKHALIDWE CHA UCHIMO? Mulungu anakonda dziko lapansi Nanapatsa mwana wake yekhayo Kuti onse okhulupirira Iye Asatayike akhale nawo moyo Ungapite kumwamba ndi chikhalidwe cha uchimo? Ayi mtima uyenera kusinthka Mtima wanga usinthe ndisanapite kumwamba. Yohane 3:16
15.
15. KODI KUSINTHA KWA MTIMA KUTCHEDWA CHIYANI? Ezekiyele 36: 26 mpaka 27 Mdzakupatsa mtima watsopano Mkati mwanu Mzimu watsopano M’dzachotsa mtima wa mwala Kukupatsani mtima wa mnofu Kukupatsani Mzimu wanga Kukuyendetsa m’malemba anga Mudzasunga maweruzo anga Ndikuwachita malemba anga Kusintha mtima mchani? Kusintha mtima kutchedwa kubadwanso Kusintha kwa mtima mmchani? Kutchedwa kubadwanso Ezekiele 36  
16.
16. ANGASINTHE MTIMA WA OCHIMWA NDANI? Palibe mpulumutsi winanso Palibe dzina lina pansi pathambo Lopatsidwa, kwa anthu kupulumutsa lnde palibe dzina lina Angasinthe mtima ndani? Mulungu yekha Mulungu yekha Mulungu yekha angasinthe mtima ochimwa Machitidwe 4 ndime 12 Palibe dzina lopatsidwa kwa anthu Limene lipulumutsa.  
17.
17. MPULUMUTSI WA OSANKHIDWA A MULUNGU NDI NDANI? Ndani ndani ndani mpulumutsi Mpulumutsi wa osankhidwa a Mulungu Ndani ndani ndani mpulumutsi Mpulumutsi waosankhidwa a Mulungu Yekhayo mpulumutsi ndiye Yesu Khristu Mwana wa muyaya wa Mulungu Anakhala munthu, komanso ali Mlungu Munthu m’modzi zilengedwe ziwiri Ndine njira, choonadi ndi moyo Palibe adza kwa Atate osadzera mwa Ine Ine ndi njira, choonadi ndi moyo Yohane 14 ndime 6  
18.
18. MTIMA WAKO USINTHA BWANJI? Mtima usintha bwanji? Mtima wanga usintha ndi Mzimu Woyera Mtima usintha bwanji? Mchisomo cha Mulungu Mtima usintha bwanji? Chooneka mntchito ya Khristu Mtima wasintha mchisomo cha Mulungu   Chifundo chikondi cha Mulungu zidaoneka Mpulumutsi wathu Adapulumutsa osachokera muntchito Mwachifundo chake Kupulumutsa mwakutsuka kwa kubadwanso Ndi makonzedwe a Mzimu Woyera Amene apereka mochurukira Khristu Mpulumutsi wathu Tito mutu 3 ndime 4, 5 ndi 6
19.
19. CHISOMO NDI CHIYANI? Ndinu anthu wopatulika wa Mulungu Ambuye Mlungu wakusankhani Ndinu mtundu wa wopatulika wa Mulungu Wosankhidwa kuchokera mdziko Chisomo mchani? Chisomo ndi chifundo cha cha Mulungu Poyenera chilango Deuteronomo 7 ndime 6
20.
20. KHRISTU ADAGWIRA NTCHITO YANJI YOKUPULUMUTSA? Mulungu anamuyesa, iye Wopanda uchimo kukhala tchimo Kukhala tchimo m’malo mwathu Kuti mwa iye tikakhale tikakhale Chiyero cha Mulungu Chiyero cha Mulungu 2 Akorinto 5 ndime 21 Khristu adatani populumutsa? Adasunga malamulo a Mulungu Nalangidwa chifukwa cha machimo anga Chifukwa cha machimo anga
21.
21. ALIPO ANGAPULUMUTSIDWE NDI NTCHITO ZAKE? Angapulumuke ndani ndi tchito zake Palibe angapulumutsidwe Ndimwachisiomo mwapulumuka Pokhulupilira osati nokha Iyi ndi mphatso ya Mulungu Aefeso 2 ndime 8 Iyi ndi mphatso yokongola  
22.
22. TIPINDULANJI KU NTCHITO YA CHRISTU? Tipindulanji ku ntchito ya Khristu? Mlungu akonzanso, ayeretsa Mlungu akozanso, ayeretsa Alungamitsa okhulupira Khristu Munasambitsidwa munayeretsedwa Munalungamitsidwa mdzina Mdzina la Ambuye Yesu Christu mwa Mzimu wa Mulungu 1 Akorinto 6 ndime 11 Mulungu, akonzanso ayeretsa 1 Akorinto 6 ndime 11 Ayeretsa okhulupira Khristu.
23.
23. KULUNGAMA NDI CHANI? Kulungama ndi chiyani? Kulungama ndipamene Mulungu akhululukira machimo onse kundipanga wangwiro Choncho palibe kutsutsidwa Onse ali mwa Yesu Khristu Aroma Mutu 8 ndime 1  
24.
24. UNALUNGAMITSIDWA BWANJI? Lungamitsiwa, lungamitsiwa lungamitsiwa Ndalungama, lungamitsidwa, lungamitsidwa Munchito ya Khristu  Chifukwa cha chiyero Chifukwa chachiyero   Ulungama bwanji? Munthu sayesedwa olungama Pantchito ya malamulo Koma mwa chikhululupiriro cha Yesu. Agalatiaya 2 ndime 6  
25.
25. KUYERETSEDWA NDI CHANI? Kuyeretsedwa ndi chiyani? Kuyeretsedwa Mulungu kundipanga wangwiro Mtima ndi khalidwe Kundiyeretsa   Mulungu wamtendere ayeretse konseko Mzimu, moyo ndi thupi lanu Zisungidwe za mphumphu. Pakubwera Ambuye wathu Yesu Khristu Wakuyitana ngokhulupirika Mlungu adzazichita 1 Atesolonika 5:23 ndi 24 Wokwiyitana ngokhulupilika Mlungu adzazichita
26.
26. MAGAWO AWIRI A CHIYERO NDI ATI? Kufa kuuchimo moyo mchiyero Kufa kuuchimo moyo mchiyero Kufa kuuchimo moyo mchiyero Magawo awiri achiyero ndi cha? Ndinapachikidwa ndi Khristu sindiri wa moyo Khristu akhala mkati mwanga Moyo wanga mthupirili ndi mwachikhulupiro mwa Khristu Nandikonda nadzipereka kwa ine Agalatiya 2 ndime 20 Ndikhala mchikhulupiriro Nandikonda nadzipereka ine Nandikonda nadzipereka ine  
27.
27. KODI KHRISTU ADAFERA NDANI? Simukhulupirira chifukwa, sinu nkhosa zanga Nkhosa zanga zimandivera Ndizidziwa, zinditsata Ndipo sizidzaonongeka Palibe wozikwatula m’dzanja langa Atate wanga wondipatsa izo ,ndi wamkulu pa onse Yohane 10 ndime 26 mpaka 29 Palibe adzazikwatula Khristu adafera nda? Adafera onse, opatsidwa kwa Iye ndi Atate  
28.
28. ADZAPULUMUTSIDWE NDIYANI? Woyipa asiye njira yake Wosalungama maganizo ake Nabwere nabwere kwa Ambuye Adzamchitira chifundo iye Adzamchitira chifundo iye Awererani kwa Mbeye, pakuti adzakhululukira Adzamchitira chifundo Yesaya 55 ndime 7 Adzapulumuka ndini? Yense olapa ndikukhulupirira Wokhulupirira Ambuye Yesu Khristu  
29.
29. KODI KULAPA NDI CHIYANI? Kodi kulapa ndi chiyani? Kulapa ndi kumva chisoni Chifukwa cha tchimo, kudana nalo ndikulisiya Chifukwa silikondweretsa Mulungu Anthu anga otchulidwa ndi dzina langa Akadzichepetsa mkupemphera Nakafuna nkhope yanga nasiya njira zoyipa Ndidzamvera ndikukhululukira Mbiri 7: 14  
30.
30. CHIKHULUPILIRO MWA KHRISTU NDI CHANI? Chikhulupiro mchiyani? Kukhulupilira Khristu Chikukhulupiliro ndikudalira Yesu yekhayo pachipulumutso Chikhulupiliro mchani Kukhulupilira Khristu Chikhulupiliro ndikudalira Yesu yekhayo Afilipi 3 ndime 9 Chiyero chochokera kwa Mulungu Pokhulupilira Khristu Wosakhala chiyero changa Chochokera mu lamulo Chomwe chili po khulupilira Khristu

credits

released January 1, 2015

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account